Masalimo 12 - Buku LopatulikaAnthu ndi amabodza, Mulungu ndiye woona Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Seminiti. Salimo la Davide. 1 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu. 2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri. 3 Yehova adzadula milomo yonse yothyasika, lilime lakudzitamandira; 4 amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani? 5 Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo. 6 Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri. 7 Mudzawasunga, Yehova, mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse. 8 Oipa amayenda mozungulirazungulira, potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi