Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 12:6 - Buku Lopatulika

6 Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Malonjezo a Chauta ndi angwiro, ali ngati siliva womkometsa m'ng'anjo yamoto, woyeretsedwa kasanunkaŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 12:6
16 Mawu Ofanana  

Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.


Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi; analanda nyumba mwachiwawa, imene sanaimange.


Koma kuli mtapo wa siliva, ndi malo a golide amene amuyenga.


Mau anu ngoyera ndithu; ndi mtumiki wanu awakonda.


Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.


Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.


Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.


Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;


ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.


Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao; omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.


Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.


Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova.


Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa