Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 12:2 - Buku Lopatulika

2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Aliyense amangonamiza mnzake, amathyasika ndi pakamwa pake, amalankhula ndi mitima iŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Aliyense amanamiza mʼbale wake; ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 12:2
25 Mawu Ofanana  

A Zebuloni akutuluka kukhamu, opangira nkhondo, monga mwa zida zilizonse za nkhondo, zikwi makumi asanu, akusunga malongosoledwe a nkhondo ndi mtima wosatekeseka.


M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.


Pofulumizidwa mtima ndinati ine, anthu onse nga mabodza.


Ndilanditseni ndi kundipulumutsa kudzanja la alendo, amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.


amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.


Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.


Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.


Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza; mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake, akanka nayenda namakanena.


Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.


Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.


Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.


Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?


Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde.


Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao.


Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.


Pakuti sikudzakhalanso masomphenya achabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israele.


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.


Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;


munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha panjira zake zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa