Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 39:1 - Buku Lopatulika

1 Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndidati, “Ndidzasamala zochita zanga, kuti ndisachimwe polankhula. Ndidzatseka pakamwa panga nthaŵi zonse pamene anthu oipa ali nane.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe; ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 39:1
21 Mawu Ofanana  

kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele.


Koma Yehu sanasamalire kuyenda m'chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.


ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha;


Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.


Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.


amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?


Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.


Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.


Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.


Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga; kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu.


Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.


Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.


Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.


Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.


Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.


Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa