Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 3:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 3:6
62 Mawu Ofanana  

Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite.


Ndipo anthu a Israele anayankha anthu a Yuda, nati, Ife tili ndi magawo khumi mwa mfumu, ndi mwa Davide koposa inu; chifukwa ninji tsono munatipeputsa ife, osayamba kupangana nafe za kubwezanso mfumu yathu? Koma mau a anthu a Yuda anali aukali koposa mau a anthu a Israele.


Ndipo Abiya ndi anthu ake anawakantha makanthidwe aakulu; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazana asanu a Israele.


Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.


Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;


Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.


Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa; ndipo m'milomo mwake muli moto wopsereza.


mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.


Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.


Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi aakulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita;


Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'chuuno ndi nsakali, yendani inu m'chilangali cha moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho cha padzanja langa; mudzagona pansi ndi chisoni.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.


ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.


popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.


Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.


Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.


Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.


ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.


Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?


naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo;


Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;


amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.


Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?


Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;


ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,


Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mau oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo.


Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.


ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.


Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa