Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 10:7 - Buku Lopatulika

7 M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pakamwa pake pamangolankhula zotemberera, zonyenga ndi zoopseza. M'kamwa mwake mumatuluka zovutitsa ena ndiponso zoipa zokhazokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza; zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 10:7
29 Mawu Ofanana  

Aima ndi chovuta, nabala mphulupulu, ndi m'mimba mwao mukonzeratu chinyengo.


Chinkana choipa chizuna m'kamwa mwake, chinkana achibisa pansi pa lilime lake;


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.


Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga, choipa cha milomo yao chiwaphimbe.


Ndilanditseni ndi kundipulumutsa kudzanja la alendo, amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.


amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.


Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.


Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza; mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake, akanka nayenda namakanena.


Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.


Pakamwa pako mpochita zochimwa, ndipo lilime lako likonza chinyengo.


ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Oipa achita chilendo chibadwire, asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.


Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.


Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza mu Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi.


Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.


Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;


Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake; anaima ndi chovuta, nabala bodza.


Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa, alankhula modzitama.


Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.


Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;


Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.


Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.


Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.


Tamverani ichi, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti,


Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa