Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 10:8 - Buku Lopatulika

8 Akhala m'molalira midzi; mobisalamo akupha munthu wosachimwa. Ambisira waumphawi nkhope yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Akhala m'molalira midzi; mobisalamo akupha munthu wosachimwa. Ambisira waumphawi nkhope yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Amalalira m'midzi, amapha anthu osalakwa m'malo obisalira. Amazondazonda kuti apeze opanda mwai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi, kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa, amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 10:8
14 Mawu Ofanana  

Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.


Kukacha auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi; ndi usiku asanduka mbala.


Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu, apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi.


Amapha wamasiye ndi mlendo, nawapha ana amasiye.


Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.


Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.


Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.


Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.


Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,


Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.


Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvala efodi wabafuta.


Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa