Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 10:9 - Buku Lopatulika

9 Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Amabisalira osauka ngati mkango m'ngaka yake, amabisalira osauka kuti aŵagwire. Osaukawo amaŵagwiradi akaŵakokera mu ukonde wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba. Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu; amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 10:9
28 Mawu Ofanana  

pamene ibwatama m'ngaka mwao, nikhala mobisala kulaliramo?


Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.


Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Afanana ndi mkango wofuna kumwetula, ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira.


Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova,


Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake; koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.


Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.


Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.


muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.


Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu.


Andikhalira chilombo cholalira kapena mkango mobisalira.


Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa.


Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwake usanagwire kanthu?


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


Aziwedza zonse ndi mbedza, azigwira mu ukonde wake, nazisonkhanitsa m'khoka mwake; chifukwa chake asekera nakondwerera.


Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.


Mau a kuchema kwa abusa! Pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! Pakuti kudzikuza kwa Yordani kwaipsidwa.


Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;


Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa