Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

119 Mau a Mulungu Okhudza Kupanduka

Mulungu ndi wapamwamba komanso woyenera ulemu, woyenera kutamandidwa konse. Pamaso pake, mapiri amanjenjemera, ndipo palibe wopanduka amene adzaperekedwa chilango. Dzina la Wamuyaya silitha; ali ndi mphamvu zosayerekezeka.

Chifukwa chake, konza zomwe zikuoneka zopindika mumtima mwako. Ngati pali choipa mumtima mwako, funa chikhululukiro kwa Mulungu, pakuti iye ndi wolungama komanso wachifundo. Usatsutse mawu ake kapena chifuniro chake, chifukwa sudzapila padziko lapansi ngati uchita zinthu mosemphana ndi zimene iye akufuna.

Lero ndi tsiku loyanjanirana naye, lotsegula mtima wako ndikudzitukumula pamaso pake, chifukwa mtima wodzichepetsa sudzatayidwa naye. Muzindikire m'njira zanu zonse ndipo musadzione ngati wanzeru pa maganizo anu, koma m'malo mwake, dalirani Mulungu ndipo musamadzikulitse; chifukwa, ngati simutero, moyo wanu udzawonongeka ndipo mudzapandukira amene anakulengani ndi kukupatsani moyo.

Njira za Mulungu ndi zangwiro ndipo zimatsogolera ku moyo wosatha, pomwe njira za munthu ndi zoyipa ndipo zimatsogolera ku imfa.


Yeremiya 28:16

Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:6

Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 15:22-23

Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.

Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 5:23

Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nachoka.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 13:5

Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, nakuombolani m'nyumba ya ukapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 20:24

Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 12:14-15

Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ake, ndi kusakana lamulo lake la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, chabwino.

Koma mukapanda kumvera mau a Yehova, ndi kupikisana ndi lamulo la Yehova, dzanja la Yehova lidzatsutsana nanu, monga linatsutsana ndi makolo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:1

Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 32:9

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza;

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 14:9

Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 9:7

Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m'dziko la Ejipito, kufikira munalowa m'malo muno munapikisana ndi Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:10

Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 63:10

Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 66:24

Ndipo iwo adzatuluka ndi kuyang'ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mphutsi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 2:19

Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 78:8

Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikike ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 1:18

Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 3:42

Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukire.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 4:17

Monga adindo a m'munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 59:2

koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 13:16

Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 33:8

Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 31:27

Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine!

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 2:3

munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 5:25

Mphulupulu zanu zachotsa zimenezi, ndi zochimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 107:11

popeza anapikisana nao mau a Mulungu, napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:2

Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 3:13

Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 15:23

Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:8

Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 59:13

ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:11

Woipa amafuna kupanduka kokha; koma adzamtumizira mthenga wankhanza.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:13

Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 2:3

Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israele, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:43

Iye anawalanditsa kawirikawiri; koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao, ndi mphulupulu zao zinawafoketsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Danieli 9:9

Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:7

Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:2

Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo aoao;

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 9:26

Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 1:26-27

Koma simunafune kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu.

Ndipo munadandaula m'mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, Iye anatitulutsa m'dziko la Ejipito, kutipereka m'manja mwa Aamori, ationonge.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:2

Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 44:16-17

Koma mau amene wanena ndi ife m'dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe.

Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 2:4

Pakuti ngati Mulungu sanalekerere angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 36:16

koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 2:29

Chifukwa chanji mudzatsutsana ndi Ine nonse? Mwandilakwira Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 4:6

Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 8:5

Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 2:19

Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 33:3

kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 81:11-12

Koma anthu anga sanamvere mau anga; ndipo Israele sanandivomere.

Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 7:24

Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 17:14-15

Koma sanamvere, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirire Yehova Mulungu wao.

Ndipo anakaniza malemba ake, ndi chipangano anachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa.

Mutu    |  Mabaibulo
Danieli 9:5

tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu;

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 48:8

Inde, iwe sunamve; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 7:13

Tsoka kwa iwowa! Pakuti anandizembera; chionongeko kwa iwowa! Pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:21

Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:9

Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 11:10

Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 31:29

Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:28

Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ochimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 25:4-5

Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ake onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvere, simunatchere khutu lanu kuti mumve;

ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 78:40

Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, nammvetsa chisoni m'chipululu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 50:5

Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhale wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 13:10

Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 23:35

Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso choipa chako ndi zigololo zako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 9:13-14

Ndipo Yehova ati, Chifukwa asiya chilamulo changa ndinachiika pamaso pao, ndipo sanamvere mau anga, osayenda m'menemo;

koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:7

Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:9

Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva chilamulo cha Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 3:7

Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 15:6

Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; chifukwa chake ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 14:1

Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 9:17

nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:24-26

Chifukwa ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira;

koma munapeputsa uphungu wanga wonse, ndi kukana kudzudzula kwanga.

Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu, ndidzatonyola pakudza mantha anu;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 12:19

Motero Aisraele anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 29:13

Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 32:33

Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 7:11-12

Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.

Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 5:24

Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 44:4-5

Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.

Koma sanamvere, sanatchere khutu lao kuti atembenuke asiye choipa chao, osafukizira milungu ina.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 3:2-4

Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,

osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,

achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 16:12

ndipo mwachita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wake woipa, kuti musandimvere Ine;

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 3:7

Koma nyumba ya Israele siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israele ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 18:12

Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:21-23

chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.

Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;

nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:12

Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 3:15

umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:32

amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 66:3-4

Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;

Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamve konse; koma anachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene sindinakondwere nacho.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 23:17

Anena chinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:26-27

Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,

koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 13:21-22

nafuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anachokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova Pokhala sunamvere mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,

koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe Iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 32:15

Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 2:2-3

Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,

Tidule zomangira zao, titaye nsinga zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 50:17

Popeza udana nacho chilangizo, nufulatira mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 24:5

Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ake omwe, chifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, nathyola chipangano cha nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 22:21

Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvere mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 33:11

Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 24:20

Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 78:10

Sanasunga chipangano cha Mulungu, nakana kuyenda m'chilamulo chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 5:3

Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 16:8

Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 7:13

Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamve; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankhe;

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:

Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa;

mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;

mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 24:13

M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 2:13

Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 12:14

Koma anachita choipa, popeza sanalunjikitse mtima wake kufuna Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:5

Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 9:9

Anadzivunditsa kwambiri, monga masiku a Gibea; adzakumbukira mphulupulu yao, adzalanga zochimwa zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 57:17

Chifukwa cha kuipa kwa kusirira kwake ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 4:6-8

Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.

Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.

M'mwemo mizinda iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumzinda umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:38

ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 19:15

Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mzinda uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 8:9

Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 25:7

Koma simunandimvere Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu ndi kuonapo choipa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:15

Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 30:8

Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ake opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 10:6

Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 3:4

Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 2:4

Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza akaniza chilamulo cha Yehova, osasunga malemba ake; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Mtima wanga ukukutamandani Mulungu Wamuyaya, manja anu andilenga ndipo munapatsa mpweya moyo wanga. Ulamuliro wanu ndi waukulu, zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi zili pansi pa mphamvu zanu. Chifukwa cha ichi, ndikupatsani ulemerero wonse chifukwa ndinu woyenera kutamandidwa. Mulungu wanga, lero ndimayimirira pamaso panu ndi mtima wodzichepetsa. Ndikufuna mundisanthule mkati mwanga ndi kunditsuka ku zoipa zanga zonse. Ngati ndakhala ndi malingaliro kapena zochita zonditsutsa inu, ndikupempha chikhululukiro. Sindikufuna kuchita chilichonse chotsutsana ndi chifuniro chanu. Chonde wongolani mapazi anga ndi kundionetsa njira yoyenera kuyendamo. Musandilole kudzidalira kwambiri kapena mtima wanga ukukutsutsani. Ndidzimasula ku malingaliro onse akundikopa kuchita zoipa. Mu dzina la Yesu, ndikukuthokozani chifukwa cha mtima woyera womwe mwandipatsa. M'dzina la Yesu, Ameni.