Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 5:3 - Buku Lopatulika

3 Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kodi Inu Chauta, suja mumafuna anthu onena zoona? Inu mudaŵakantha anthuwo, koma iwo sadamve kuŵaŵa. Mudaŵatswanya, koma sadafune kutembenuka mtima. Adaumitsa mitima yao ngati mwala, adakana kwamtuwagalu kulapa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona? Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka; munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala ndipo anakaniratu kulapa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:3
45 Mawu Ofanana  

Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu.


Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere panjira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje.


Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.


Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.


Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.


Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.


Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera, kuti mafupawo munawathyola akondwere.


Anatulutsa manja ake awagwire iwo akuyanjana naye, anaipsa pangano lake.


Munthu woipa aumitsa nkhope yake; koma woongoka mtima akonza njira zake.


Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa; koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.


Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; anandikwapula, osamva ine; ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafunafunanso vinyoyo.


Ungakhale ukonola chitsiru m'mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale, koma utsiru wake sudzamchoka.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m'mtima.


Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;


Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.


Ndawapeta ndi chopetera m'zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.


koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve asalandire langizo.


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mzinda uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.


Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.


Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.


wamkulu mu upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala mu Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga? Ati Yehova.


Sanadzichepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'chilamulo changa, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.


koma sanandimvere Ine sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.


Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao.


Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.


Ndipo anawa, ndiwo achipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nao, Atero Yehova Mulungu.


M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.


Monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose choipa ichi chonse chatidzera; koma sitinapepese Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kuchita mwanzeru m'choonadi chanu.


Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;


Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


M'mwemo mizinda iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumzinda umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pake pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, navunditsa machitidwe ao onse.


Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere.


Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa