Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:21 - Buku Lopatulika

21 Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvere mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvera mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ndidaakuchenjezani pamene zinthu zinkakuyenderani bwino. Koma inu mudati, ‘Sitidzamvera.’ Ndi m'mene mwakhala mukuchitira kuyambira muli ana aang'ono, simudamvere mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere. Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’ Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono. Simunandimvere Ine.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:21
35 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ake, koma sanasamalire.


Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.


Inde, iwe sunamve; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.


Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mzinda uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.


Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.


Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?


Kuyambira chaka chakhumi ndi chitatu cha Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunena; koma simunamvere.


Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ake onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvere, simunatchere khutu lanu kuti mumve;


Koma simunandimvere Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu ndi kuonapo choipa inu.


Chifukwa chake Yehova wa makamu atero: Popeza simunamvere mau anga,


Ndipo chochititsa manyazi chinathetsa ntchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao aamuna ndi aakazi.


Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.


Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.


Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchere khutu lanu, simunandimvere Ine.


Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.


Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.


Sanamvera mau, sanalole kulangizidwa; sanakhulupirire Yehova, sanayandikire kwa Mulungu wake.


Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'mizinda mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo?


Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine!


Munakhala opikisana ndi Yehova kuyambira tsikuli ndinakudziwani.


Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m'dziko la Ejipito, kufikira munalowa m'malo muno munapikisana ndi Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa