Eksodo 16:8 - Buku Lopatulika8 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Ndipo Mose adati, “Ndi Chauta amene adzakupatsani madzulo nyama yoti mudye, ndi m'maŵa buledi woti nkukhuta, chifukwa choti wamva madandaulo anu onse omuŵiringulira aja. Ife ndife yani? Madandaulo anu simudaŵiringulire ife ai, koma Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.” Onani mutuwo |