Yeremiya 18:12 - Buku Lopatulika12 Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 “Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nzopanda pake. Tidzachita monga m'mene tifunira, ndipo aliyense mwa ife azidzangotsata zoipa za mtima wake wokanika.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ” Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.