Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 4:17 - Buku Lopatulika

17 Monga adindo a m'munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Monga adindo a m'munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Akuzinga Yerusalemu ngati alonda a munda, chifukwa choti anthu andipandukira,” akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda, chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:17
16 Mawu Ofanana  

Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.


Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.


Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati chitando cha m'munda wampesa, chilindo cha m'munda waminkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.


Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva chilamulo cha Yehova;


Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nachoka.


Ndipo panaoneka chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anafika, iye ndi nkhondo yake, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zithando; ndipo anammangira malinga pozungulira pake.


Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.


Yerusalemu wachimwa kwambiri; chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa; onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche; inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.


Munakhala opikisana ndi Yehova kuyambira tsikuli ndinakudziwani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa