Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 106:7 - Buku Lopatulika

7 Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu m'Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamene makolo athu anali ku Ejipito, sadasamale ntchito zanu zodabwitsa. Sadakumbukire kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, koma adaukira Mulungu Wopambanazonse ku Nyanja Yofiira kuja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pamene makolo athu anali mu Igupto, sanalingalire za zozizwitsa zanu; iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka, ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 106:7
19 Mawu Ofanana  

Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita; zizindikiro zake ndi maweruzo a pakamwa pake;


Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.


Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.


Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.


Ndipo anaiwala zochita Iye, ndi zodabwitsa zake zimene anawaonetsa.


Sanakumbukire dzanja lake, tsikuli anawaombola kwa msautsi.


Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?


Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.


Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.


Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.


Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake.


kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.


Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja;


Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.


koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa