Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 3:13 - Buku Lopatulika

13 Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvera mau anga, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ungovomera kulakwa kwako. Vomera kuti udaukira Chauta Mulungu wako, kuti udapembedza nao milungu yachilendo patsinde pa mitengo yogudira, ndiponso kuti sudamvere mau anga,’ ” akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ungovomera kulakwa kwako kuti unawukira Yehova Mulungu wako. Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndiponso kuti sunandimvere,’ ” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 3:13
22 Mawu Ofanana  

Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.


Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.


Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?


Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao.


Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu.


Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.


Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.


Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagone ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.


Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.


Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri aatali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.


Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.


koma sanandimvere Ine sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.


Koma unatama kukongola kwako, ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo; unali wake.


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa