Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 3:14 - Buku Lopatulika

14 Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzimmodzi wa pa mzinda uliwonse, ndi awiriawiri a pa banja lililonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzimmodzi wa pa mudzi uliwonse, ndi awiriawiri a pa banja lililonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Bwererani inu anthu osakhulupirika, pakuti mbuye wanu ndine. Ndidzakutengani kupita nanu ku Ziyoni, mmodzi kuchokera ku mzinda uliwonse, aŵiri kuchokera ku banja lililonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 3:14
31 Mawu Ofanana  

Tsono amtokoma anamuka ndi makalata ofuma kwa mfumu ndi akulu ake mwa Israele ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israele, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Israele, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asiriya.


Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.


Popeza ngakhale anthu anu Israele akunga mchenga wa kunyanja, otsala ao okhaokha adzabwera; chionongeko chatsimikizidwa chilungamo chake chisefukira.


Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo wa azitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.


Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israele inu.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.


woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.


Chifukwa cha kuipa kwa kusirira kwake ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wake.


Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.


Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.


Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipirikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso kumakola ao; ndipo zidzabalana ndi kuchuluka.


Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupirikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.


Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.


Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse.


Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.


Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni.


si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.


Pakuti lidzafika tsiku, limene alonda a pa mapiri a Efuremu adzafuula, Ukani inu, tikwere ku Ziyoni kwa Yehova Mulungu wathu.


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova.


Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa