Masalimo 2 - Buku LopatulikaUfumu wa wodzozedwa wa Yehova 1 Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake? 2 Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti, 3 Tidule zomangira zao, titaye nsinga zao. 4 Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza. 5 Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake, nadzawaopsa mu ukali wake. 6 Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera. 7 Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala. 8 Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako. 9 Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba. 10 Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi. 11 Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe. 12 Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi