Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 2:4 - Buku Lopatulika

4 Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chauta amene amalamulira kumwambako akungoŵaseka ndi kuŵanyoza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 2:4
13 Mawu Ofanana  

Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; achita chilichonse chimkonda.


Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.


Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.


Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.


Koma Inu, Yehova, mudzawaseka; mudzalalatira amitundu onse.


Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga.


Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe; taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.


Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu, ndidzatonyola pakudza mantha anu;


Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa