Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero


Salimo 2

1 Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu?

2 Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo.

3 Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.”

4 Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo.

5 Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,

6 “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.”

7 Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako.

8 Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.

9 Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”

10 Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.

11 Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.

12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.

The Word of God in Contemporary Chichewa

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®

Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®

Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Biblica, Inc.
Titsatireni:



Zotsatsa