Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 2:10 - Buku Lopatulika

10 Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nchifukwa chake tsono khalani anzeru, inu mafumu. Chenjerani inu amene muli olamula dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 2:10
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.


Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.


Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.


Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Ndipo kudzachitika kuti aliyense wa mabanja a dziko wosakwera kunka ku Yerusalemu kulambira mfumu Yehova wa makamu, pa iwowa sipadzakhala mvula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa