Miyambo 1 - Buku LopatulikaZochitira miyambo 1 Miyambo ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele. 2 Kudziwa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mau ozindikiritsa; 3 kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika; 4 kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira; 5 kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira; ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu; 6 kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake, mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao. Munthu asalole oipa amchete 7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo. 8 Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amai ako; 9 pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako, ndi mkanda pakhosi pako. 10 Mwananga, akakukopa ochimwa usalole. 11 Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi, tilalire osachimwa opanda chifukwa; 12 tiwameze ali ndi moyo ngati manda, ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje; 13 tidzapeza chuma chonse cha mtengo wake, tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha; 14 udzachita nafe maere, tonse tidzakhala ndi chotengeramo chimodzi. 15 Mwananga, usayende nao m'njira; letsa phazi lako ku mayendedwe ao; 16 pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi. 17 Pakuti kutchera msampha pamaso pa mbalame ndi chabe; 18 ndipo awa abisalira mwazi waowao, alalira miyoyo yaoyao. 19 Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere; chilanda moyo wa eni ake. Chenjezo la Nzeru 20 Nzeru ifuula panja; imveketsa mau ake pabwalo; 21 iitana posonkhana anthu polowera pachipata; m'mzinda inena mau ake, 22 Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru? 23 Tembenukani pamene ndikudzudzulani; taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, ndikudziwitsani mau anga. 24 Chifukwa ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira; 25 koma munapeputsa uphungu wanga wonse, ndi kukana kudzudzula kwanga. 26 Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu, ndidzatonyola pakudza mantha anu; 27 pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula, ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu; pakudza kwa inu vuto ndi nsautso. 28 Pamenepo adzandiitana, koma sindidzavomera; adzandifunatu, osandipeza ai; 29 chifukwa anada nzeru, sanafune kuopa Yehova; 30 anakana uphungu wanga, nanyoza kudzudzula kwanga konse; 31 momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao. 32 Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga. 33 Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phee osaopa zoipa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi