Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 13:16 - Buku Lopatulika

16 Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 A ku Samariya adzalangidwa chifukwa choti adapandukira Mulungu wao. Adzaphedwa ndi lupanga, ana ao adzaphedwa moŵakankhanthitsa pansi. Akazi ake apathupi adzang'ambidwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo, chifukwa anawukira Mulungu wawo. Adzaphedwa ndi lupanga; ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi, akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 13:16
23 Mawu Ofanana  

Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.


Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha.


Pamenepo mfumu ya Asiriya anakwera m'dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu.


Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'mizinda ya Amedi.


Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.


Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa.


Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu.


Chifukwa kuti mwana asanakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.


Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.


Ndi lupanga lidzagwera mizinda yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;


Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero aakulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.


Ndinaona Ambuye alikuima paguwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi.


Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang'ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetsereka.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ake a makanda anaphwanyika polekeza pake pa miseu yake yonse; ndi pa omveka ake anachita maere, ndi akulu ake onse anamangidwa maunyolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa