Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 2:19 - Buku Lopatulika

19 Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Choipa chako dzidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mudzalangidwa ndi machimo anu omwe: poti mwandikana, ndidzakuimbani mlandu. Muganizire bwino za kuipa kwake kwa kundisiya Ine, Chauta, Mulungu wanu. Mulingalire kuŵaŵa kwake kwa kukhala osandiwopa,” akuterotu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Kuyipa kwanuko kudzakulangani; kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani. Tsono ganizirani bwino, popeza ndi chinthu choyipa kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu; ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu. Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:19
40 Mawu Ofanana  

Nati iye, Sindimavute Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.


Pamenepo Semaya mneneri anadza kwa Rehobowamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, chifukwa chake Inenso ndasiya inu m'dzanja la Sisake.


Chinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lake; chifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.


Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake.


Ndipo ana a Israele anazichotsera zokometsera zao kuyambira paphiri la Horebu.


momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao.


Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.


Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.


Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.


Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;


Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao.


Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zitendene zako zaphwetekwa.


Kodi sunadzichitire ichi iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira?


Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.


Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako.


Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.


Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yake; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.


Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.


Kodi autsa mkwiyo wanga? Ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?


Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.


Izi adzakuchitira chifukwa watsata amitundu, ndi kuchita nao chigololo, popezanso wadetsedwa ndi mafano ao.


Ndinachita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.


Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.


Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako.


Israele, bwerera kunka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.


Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.


Ndipo kudzikuza kwa Israele kudzamchitira umboni pamaso pake; chifukwa chake Israele ndi Efuremu adzakhumudwa m'mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao.


Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.


Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.


Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.


Chichitika ichi chonse chifukwa cha kulakwa kwa Yakobo, ndi machimo a nyumba ya Israele. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? Ndi misanje ya Yuda ndi iti? Si ndiyo Yerusalemu?


Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.


kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.


Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu ina, chifukwa chake sindikupulumutsaninso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa