Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

90 Mau a Mulungu Okhudza Kumulemekeza


Masalimo 111:10

Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:7

Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 89:7

Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:28-29

Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.

Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 96:9

Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa, njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:7

Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa;

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 12:13

Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 8:13

Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akuchititseni mantha Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:9

Opani Yehova, inu oyera mtima ake; chifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 147:11

Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:27

Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo, kupatutsa kumisampha ya imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 10:12-13

Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,

kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:14

Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye; ndipo adzawadziwitsa pangano lake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:120

Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:1

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:161

Nduna zinandilondola kopanda chifukwa; koma mtima wanga uchita nao mantha mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:20

Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa Iye kukhale pamaso panu, kuti musachimwe

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 1:50

Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuopa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:19

Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 10:12

Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:10-11

kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,

ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:23

Kuopa Yehova kupatsa moyo; wokhala nako adzakhala wokhuta; zoipa sizidzamgwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:11

Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:17

Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 2:11

Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 111:5

Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:33

Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 66:2

Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:23-24

chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;

podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:7

Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:17

Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 115:11

Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova; ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 28:28

Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:41

Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:38

Limbitsirani mtumiki wanu mau anu, ndiye wodzipereka kukuopani.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:16

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 8:13

Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:10

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:57

Yehova ndiye gawo langa: Ndinati ndidzasunga mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 147:10-11

Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu.

Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:27

Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 111:1

Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 33:6

Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:2

Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; koma wokhota m'njira yake amnyoza.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 5:29

Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 4:4

Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 5:7

Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:11

Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:11

Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 57:15

Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1

Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:74

Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera; popeza ndayembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 111:9

Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:7

Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 33:8

Dziko lonse lapansi liope Yehova, ponse pali anthu achite mantha chifukwa cha Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 11:3

ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:28

Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:17

Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 9:10

Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziwa Woyerayo ndiko luntha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:4

Imbirani Yehova, inu okondedwa ake, ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 50:10

Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:13

ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:29

chifukwa anada nzeru, sanafune kuopa Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:23-24

Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.

Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 16:29

Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 22:23

Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:6

Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:4

Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 33:18

Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:9

Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 76:7

Inu ndinu woopsa; ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 11:20

Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 101:3

Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:1

Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 149:5

Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 104:31

Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha; Yehova akondwere mu ntchito zake;

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:12

pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:30-31

Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu:

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:7

Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:26

Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:4

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:10

Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 12:14

Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ake, ndi kusakana lamulo lake la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:7

Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 3:18

kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:157

Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri; koma sindinapatukane nazo mboni zanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 51:12

Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 149:1

Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:113

Ndidana nao a mitima iwiri; koma ndikonda chilamulo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo