Masalimo 115 - Buku LopatulikaMulungu ndi wa ulemerero, mafano ndiwo achabe 1 Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu. 2 Aneneranji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? 3 Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; achita chilichonse chimkonda. 4 Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu. 5 Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; 6 makutu ali nao, koma osamva; mphuno ali nazo, koma osanunkhiza; 7 manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao. 8 Adzafanana nao iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira. 9 Israele, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao. 10 Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao, ndi chikopa chao. 11 Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova; ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao. 12 Yehova watikumbukira; adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israele; adzadalitsa nyumba ya Aroni. 13 Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, aang'ono ndi aakulu. 14 Yehova akuonjezereni dalitso, inu ndi ana anu. 15 Odalitsika inu a kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi. 16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu. 17 Akufa salemekeza Yehova, kapena aliyense wakutsikira kuli chete: 18 Koma ife tidzalemekeza Yehova kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi