Masalimo 115:4 - Buku Lopatulika4 Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide, opangidwa ndi manja a anthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. Onani mutuwo |
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.