Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 115:14 - Buku Lopatulika

14 Yehova akuonjezereni dalitso, inu ndi ana anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Yehova akuonjezereni dalitso, inu ndi ana anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Chauta akudalitseni inu, pamodzi ndi zidzukulu zanu zomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Yehova akuwonjezereni madalitso; inuyo pamodzi ndi ana anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 115:14
19 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.


Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.


Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?


M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israele adzaphuka ndi kuchita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso padziko lonse lapansi.


Ambuye Yehova amene asonkhanitsa otayika a Israele ati, Komabe ndidzasonkhanitsa ena kwa iye, pamodzi ndi osonkhanitsidwa akeake.


Ndipo padzatuluka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzachulukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawachitiranso ulemu, sadzachepa.


Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.


Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.


Ndidzawaimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzachuluka monga anachulukira kale.


Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.


Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.


Yehova Mulungu wa makolo anu, achulukitsire chiwerengero chanu chalero ndi chikwi chimodzi, nakudalitseni monga Iye ananena nanu!


Ndipo ndinamva chiwerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israele.


Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m'manja mwao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa