Masalimo 76 - Buku LopatulikaUlemerero ndi mphamvu ya Mulungu Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Asafu. Nyimbo. 1 Mulungu adziwika mwa Yuda, dzina lake limveka mwa Israele. 2 Msasa wake unali mu Salemu, ndipo pokhala Iye mu Ziyoni. 3 Pomwepo anathyola mivi ya pauta; chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo. 4 Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka wakuposa mapiri muli achifwamba. 5 Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao; amuna onse amphamvu asowa manja ao. 6 Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo, galeta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo. 7 Inu ndinu woopsa; ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu? 8 Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba; dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete, 9 pakuuka Mulungu kuti aweruze, kuti apulumutse ofatsa onse a padziko lapansi. 10 Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa. 11 Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo; onse akumzinga abwere nacho chopereka cha kwa Iye amene ayenera kumuopa. 12 Iye adzadula mzimu wa akulu; akhala woopsa kwa mafumu a padziko lapansi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi