Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 76:11 - Buku Lopatulika

11 Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo; onse akumzinga abwere nacho chopereka cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo; onse akumzinga abwere nacho chopereka cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Lumbirani kwa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muchitedi zimene mwalumbirazo. Onse omzungulira abwere ndi mphatso kwa Iye amene ayenera kumuwopa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse; anthu onse omuzungulira abweretse mphatso kwa Iye amene ayenera kuopedwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 76:11
9 Mawu Ofanana  

Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.


Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.


Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako.


Chifukwa cha Kachisi wanu wa mu Yerusalemu mafumu adzabwera nacho chaufulu kukupatsani.


Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.


Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake.


Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa