Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 76:12 - Buku Lopatulika

12 Iye adzadula mzimu wa akulu; akhala woopsa kwa mafumu a padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Iye adzadula mzimu wa akulu; akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 ndiye amene amathetsa mphamvu akalonga ndipo amaopsa mafumu a pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Iye amaswa mzimu wa olamulira; amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 76:12
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m'matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo.


Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi.


Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake, nadzawaopsa mu ukali wake.


Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.


Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako.


Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.


Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.


Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu lakumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi.


pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.


Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; mizinda yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.


Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.


Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa