Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 76:10 - Buku Lopatulika

10 Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Zoonadi, mkwiyo wa anthu umabweretsa ulemu kwa Inu, opulumuka ku mkwiyowo mumaŵasunga pafupi ndi Inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 76:10
20 Mawu Ofanana  

Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.


Munaika malire kuti asapitirireko; kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.


Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.


Amitundu anapokosera, maufumu anagwedezeka, ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.


Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja, kukuntha kwa mafunde ake, ndi phokoso la mitundu ya anthu.


Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi; pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.


Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.


Pilato anayankha, Chimene ndalemba, ndalemba.


Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe padziko lonse lapansi.


Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa