Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 76:8 - Buku Lopatulika

8 Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba; dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba; dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chiweruzo chanu mudachilengeza kumwamba, anthu a pa dziko lapansi adaopa nakhala chete,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo, ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 76:8
16 Mawu Ofanana  

Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo.


Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.


Njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi, dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.


ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;


Kulamulira ndi kuopsa kuli ndi Iye; achita mtendere pa zam'mwamba zake.


Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.


Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?


Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.


Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.


Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.


Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m'mipita mwao zinathirana ndi Sisera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa