Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 86:11 - Buku Lopatulika

11 Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta, kuti ndiziyenda m'zoona zanu. Mundipatse mtima wosagaŵikana, kuti ndiziwopa dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndiphunzitseni njira yanu Yehova, ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu; patseni mtima wosagawikana kuti ndilemekeze dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 86:11
27 Mawu Ofanana  

Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu, ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.


Ndinasankha njira yokhulupirika; ndinaika maweruzo anu pamaso panga.


Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; ndidzaisunga kufikira kutha kwake.


Manja anu anandilenga nandiumba; mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.


Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.


Pakuti chifundo chanu chili pamaso panga; ndipo ndayenda m'choona chanu.


Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere panjira yachidikha, chifukwa cha adani anga.


Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.


Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.


Efuremu adzati, Ndili ndi chiyaninso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndili ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zochokera kwa Ine.


ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;


Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeke m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.


Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;


Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.


Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.


Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.


ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu;


Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.


Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa