Masalimo 130 - Buku LopatulikaPemphero lakuti akhululukidwe Nyimbo yokwerera. 1 M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova. 2 Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga. 3 Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? 4 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni. 5 Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira, ndiyembekeza mau ake. 6 Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha. 7 Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo. 8 Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi