Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 130:7 - Buku Lopatulika

7 Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yembekeza Yehova, iwe Israeli, pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 130:7
18 Mawu Ofanana  

Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.


Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.


Israele, uyembekezere Yehova, kuyambira tsopano kufikira kosatha.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.


Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.


Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.


woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.


Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.


Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo.


Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?


Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa