Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 130:2 - Buku Lopatulika

2 Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ambuye imvani liwu langa. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ambuye imvani mawu anga. Makutu anu akhale tcheru kumva kupempha chifundo kwanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 130:2
13 Mawu Ofanana  

Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.


Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.


mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.


Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.


Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.


Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.


M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.


Imvani Mulungu, mau anga, m'kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani.


Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Senakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa