Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


95 Mautheni a za Machiritso a Mtima

95 Mautheni a za Machiritso a Mtima


Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:5

Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:19

chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:12

Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:8

Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:1

Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:10

Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:14

Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:12-13

Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:24

Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:25-26

Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake? Kotero ngati simungathe ngakhale chaching'onong'ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:13

Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima mu Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:12

Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:11

Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:1-4

Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse; amene aombola moyo wako ungaonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:10

ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:11

Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:5

Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:35-37

Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi? Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha. Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:16

Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:20

m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:6

M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:13

Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:18

Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:15-16

Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:2

Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:13

pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:22

Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:34

Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1-2

Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:18

Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:1-3

Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera. Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu. Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake. Yerusalemu, lemekezani Yehova; Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu. Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu: Anadalitsa ana anu m'kati mwanu. Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere; akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino. Atumiza lamulo lake kudziko lapansi; mau ake athamanga liwiro. Apatsa chipale chofewa ngati ubweya; awaza chisanu ngati phulusa. Aponya matalala ake ngati zidutsu: Adzaima ndani pa kuzizira kwake? Atumiza mau ake nazisungunula; aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake. Aonetsa mau ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele. Yehova amanga Yerusalemu; asokolotsa otayika a Israele. Sanatero nao anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe. Aleluya. Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:2

Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:2-4

Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse; amene aombola moyo wako ungaonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10

Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:16-17

Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo; pakuti ndili wounguluma ndi wozunzika. Masautso a mtima wanga akula, munditulutse m'zondipsinja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:8-9

ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:4

Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:16-18

Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:4

Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:1-3

Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu. Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire. Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima. Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova. Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa. Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede. Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova. Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga. Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga. Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:1

Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:6

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:25

Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mau abwino aukondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:17

Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 3:3

Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:11

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:14

Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1-3

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende; Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo. Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse. ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro; ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:27

Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1-3

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:2-4

Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi. pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:5-6

M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova. Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:11

Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:36

Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:19

Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:5-6

Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa