Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 6:19 - Buku Lopatulika

19 chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 6:19
33 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani? Chiyembekezo changa chili pa Inu.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.


Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;


ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.


Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.


Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;


Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.


Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuche.


Ndipo m'mene anataya anangula anawasiya m'nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikulu, analunjikitsa kumchenga.


Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;


Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere.


ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:


Ndipo tsopano zitsala zitatu izi: chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.


Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.


ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Khristu Yesu;


kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;


Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu.


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.


Koma m'kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri;


koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa