Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 14:1 - Buku Lopatulika

1 Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 14:1
37 Mawu Ofanana  

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


Ndipo ndinati, Chindiwawa ichi; koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.


Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.


Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.


Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini,


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Koma Yesu anafuula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine.


Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.


Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.


Ndipo izi adzachita, chifukwa sanadziwe Atate, kapena Ine.


Koma chifukwa ndalankhula izi ndi inu chisoni chadzala mumtima mwanu.


kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye.


Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.


kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.


Mwa ichi inenso, m'mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima onse,


kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa