Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 91:4 - Buku Lopatulika

4 Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Adzakuphimba ndi nthenga zake, ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo; kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 91:4
14 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.


Ndisungeni monga kamwana ka m'diso, ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,


Gwirani chikopa chotchinjiriza, ukani kundithandiza.


Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.


Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.


Monga mphungu ikasula chisa chake, nikapakapa pa ana ake, Iye anayala mapiko ake, nawalandira, nawanyamula pa mapiko ake.


m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;


Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa