Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:6 - Buku Lopatulika

6 M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva m'Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize. Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:6
17 Mawu Ofanana  

M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.


Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba.


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.


Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Mantha ndi kunjenjemera zandidzera, ndipo zoopsetsa zandikuta.


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.


Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.


Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa