Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:7 - Buku Lopatulika

7 Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko a mapiri nawonso adanjenjemera ndi kugwedezeka, chifukwa Iye adaakalipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, ndipo maziko a mapiri anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:7
18 Mawu Ofanana  

Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.


Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.


Ndiloleni, kuti nditsitsimuke, ndisanamuke ndi kukhala kuli zii.


Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.


Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.


Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka.


Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.


Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.


Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.


Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.


Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.


Yehova, muja mudatuluka mu Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa