Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:8 - Buku Lopatulika

8 Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 M'mphuno mwake munkafuka utsi, m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga, makala amoto anali laŵilaŵi kuchokera m'kamwa momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:8
18 Mawu Ofanana  

ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.


M'kamwa mwake mutuluka miuni, mbaliwali za moto zibukamo.


amene apenyerera padziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka.


Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa.


Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.


Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?


Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.


Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.


Ndipo panatuluka moto pamaso pa Yehova, nuwatha, nafa iwo pamaso ya Yehova.


Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.


Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.


Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.


Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa