Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.
Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.
Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa, njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.
Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.
Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa Iye kukhale pamaso panu, kuti musachimwe
Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,
kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.
Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.
Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.
Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu. Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.
Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!
Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.
Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.
Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu.
Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.
ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:
Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.
Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.
Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.
Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.
Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.
Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:
Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.
Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.
Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ake, ndi kusakana lamulo lake la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, chabwino.
Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.
Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.