Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

91 Mau a m'Baibulo Othana ndi Mantha


Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:3

Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:4

Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:6

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:2

Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;

umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:34

Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:14

Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:18

Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:19

Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:6

Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.

Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?

Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:14

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:10

ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:29

Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:24

Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:23

tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:5

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:26

Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 17:20

Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:13

Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 4:20-21

ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeke chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,

nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:11

Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa; munthu adzandichitanji?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 1:3-4

Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,

wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 28:7

Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:2

Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:26

pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:6

M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:5

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:5

Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira, ndiyembekeza mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:3

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:50

Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mau anu anandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:30

Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:8

Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:37

Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:23

Koma ndikhala ndi Inu chikhalire, mwandigwira dzanja langa la manja.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:143

Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 38:15

Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova; Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:10

Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:10

kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:57

koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:5

Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:4

Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 50:7

Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:14

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:5

Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika, Mulungu adzauthandiza mbandakucha.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:14

Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:2

Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:10

Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:2

Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:18

Pamene ndinati, Literereka phazi langa, chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:31

Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:4

Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 32:7

Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:25

Maso ako ayang'ane m'tsogolo, zikope zako zipenye moongoka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:32

Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'chuuno, nakonza njira yanga ikhale yangwiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:5

Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 20:17

Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chilimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:5

Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, nimunaika dzanja lanu pa ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:1

Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 54:4

Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga, Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:3

Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:22

Koma Yehova wakhala msanje wanga; ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:28

Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:10

Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:8

Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:11

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:1

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo