Mtima wanga uli ndi chikhulupiriro, kukhulupirira zinthu zomwe sindiziona ndi maso anga. Ndimakondwera podziwa kuti Mulungu amasangalala ndi chikhulupiriro changa, pakuti Mawu ake amati popanda chikhulupiriro sitingakondweretse Mulungu. Ndili mwana wa Mulungu, ndimayenda ndi chikhulupiriro, ndikukhulupirira malonjezo a Atate wanga wakumwamba.
Ndi chikhulupiriro ndapeza chipulumutso mwa Khristu. Kuti upulumuke, uyenera kukhulupirira kuti Mulungu aliko, ndipo alikodi ngati mpweya womwe timapuma. Ndi mwa chisomo ndi chikhulupiriro momwe tingalandire Yesu ngati Ambuye wathu, kuchoka mu mdima kulowa mu kuunika kwake kodabwitsa.
Tsiku lililonse, pemphani Yesu kuti akuwonjezere chikhulupiriro chako. Ngati uli ndi kukayikira, werenga Mawu a Mulungu ndipo pemphera mu Mzimu kuti maganizo ako achepe, kuti usakhale ndi moyo wotsatira zomwe waona, koma motsatira zomwe Mulungu wanena. Ukamachita izi, udzakhala wokonzeka ndi mtima wosangalala pa tsiku limene Mulungu adzabwera kudzakutengera kumwamba pamodzi ndi Khristu Yesu.
Konda Mulungu ndi mtima wako wonse, mfunefune ndi moyo wako wonse. Mukamamufunafuna mozama kwambiri, simudzakhalanso ndi nthawi yokayikira za iye, ndipo mzimu wako udzakhala wotetezeka mwa iye.
Taonani, moyo wake udzikuza, wosaongoka m'kati mwake; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.
Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.
Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.
Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsate chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;
Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;
Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;
Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.
Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.
Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:
Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;
ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana; pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu;
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti onse akumkhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ao, mwa dzina lake.
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.
Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.
Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.
Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire mu kusakhulupirira, adzawalumikizanso, pakuti Mulungu ali wamphamvu yakutha kuwalumikizanso.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Pakuti ngati iwo a lamulo akhala olowa nyumba, pamenepo chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndimo lonjezo layesedwa lopanda pake;
Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.
Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi;
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu. Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu aliyense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupirira kuti chimene achinena chichitidwa, adzakhala nacho. Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.
amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye, ozika mizu ndi omangiririka mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.
ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeke chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.
Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira munthu. Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu.
Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.
Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu. Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.