Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 14:6 - Buku Lopatulika

6 Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 14:6
57 Mawu Ofanana  

Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


Mwa Iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.


Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa.


Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.


Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.


Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndili ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.


Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.


Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.


Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.


Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.


Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.


Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.


Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.


ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.


ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.


Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.


napempha kwa iye makalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.


kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.


kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.


Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.


kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.


ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la Khristu.


pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,


Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero.


kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.


Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili;


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi.


Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wovomereza Mwana ali ndi Atatenso.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.


Yense wakupitirira, wosakhala m'chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m'chiphunzitso, iyeyo ali nao Atate ndi Mwana.


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.


Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa