Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 17:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 17:20
19 Mawu Ofanana  

Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pake;


Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.


Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.


Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoze bwanji kuchitulutsa?


Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.


Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.


Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu.


Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu aliyense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupirira kuti chimene achinena chichitidwa, adzakhala nacho.


Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ichepa ndi mbeu zonse za padziko,


Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.


Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.


Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.


Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.


Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?


kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo;


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanathe kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa