Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 17:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo m'mene anali kutsotsa mu Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Tsiku lina ophunzira atasonkhana onse ku Galileya, Yesu adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 17:22
21 Mawu Ofanana  

Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.


koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.


ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.


Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.


Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.


Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.


Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.


Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.


Kodi sanayenere Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake?


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.


Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,


Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;


Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa